Isaiah 47

Kugwa kwa Babuloni

1“Tsika, ndi kukhala pa fumbi,
iwe namwali, Babuloni;
khala pansi wopanda mpando waufumu,
iwe namwali, Kaldeya
pakuti sadzakutchulanso wanthete kapena woyenera
kumugwira mosamala.
2Tenga mphero ndipo upere ufa;
chotsa nsalu yako yophimba nkhope
kwinya chovala chako mpaka ntchafu
ndipo woloka mitsinje.
3Maliseche ako adzakhala poyera
ndipo udzachita manyazi.
Ndidzabwezera chilango
ndipo palibe amene adzandiletse.”

4Woyerayo wa Israeli ndiye Mpulumutsi wathu,
dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.

5“Khala chete, ndipo lowa mu mdima,
iwe namwali, Kaldeya;
chifukwa sadzakutchulanso
mfumukazi ya maufumu.
6Ndinawakwiyira anthu anga,
osawasamalanso.
Ndinawapereka manja mwako,
ndipo iwe sunawachitire chifundo.
Iwe unachitira nkhanza
ngakhale nkhalamba.
7Iwe unati, ‘Ine ndidzakhalapo nthawi zonse
ngati mfumukazi.’
Koma sunaganizire zinthu izi
kapena kusinkhasinkha za mmene ziti zidzathere.

8“Ndipo tsopano, tamvera, iwe wongokonda zokondweretsawe,
amene ukukhala mosatekesekawe,
umaganiza mu mtima mwako kuti,
‘Ine ndi Ine, ndipo kupatula ine palibenso wina.
Sindidzakhala konse mkazi wamasiye,
ndipo ana anga sadzamwalira.’
9Koma mʼkamphindi, ndiponso tsiku limodzi,
zinthu ziwiri izi zidzakuchitikira:
ana ako kukufera komanso kukhala mkazi wamasiye.
Zimenezi zidzakuchitikira kwathunthu
ngakhale ali ndi amatsenga ambiri
ndi mawula amphamvu.
10Iwe unkadalira kuyipa kwako
ndipo unati, ‘Palibe amene akundiona.’
Kuchenjera ndi nzeru zako zidzakusokoneza,
choncho ukuganiza mu mtima mwako kuti,
‘Ine ndine basi, ndipo kupatula ine palibenso wina.’
11Ngozi yayikulu idzakugwera
ndipo sudzadziwa momwe ungayipewere ndi matsenga ako.
Mavuto adzakugwera
ndipo sudzatha kuwachotsa;
chipasupasu chimene iwe sukuchidziwa
chidzakugwera mwadzidzidzi.

12“Pitiriza tsono kukhala ndi matsenga ako,
pamodzi ndi nyanga zako zochulukazo,
wakhala ukuzigwiritsa ntchito kuyambira ubwana wako.
Mwina udzatha kupambana
kapena kuopsezera nazo adani ako.
13Malangizo onse amene unalandira angokutopetsa basi!
Abwere patsogolopa anthu amene amatanthauzira za kumwamba kuti adzakupulumutseni.
Abwere amene amayangʼana nyenyezi, ndi kumalosera mwezi ndi mwezi
zimene ziti zidzakuchitikire.
14Ndithudi, anthuwo ali ngati phesi;
adzapsa ndi moto.
Sangathe kudzipulumutsa okha
ku mphamvu ya malawi a moto.
Awa si makala a moto woti wina nʼkuwotha;
kapena moto woti wina nʼkuwukhalira pafupi.
15Umu ndi mmene adzachitire amatsenga,
anthu amene wakhala ukugwira nawo ntchito
ndi kuchita nawo malonda chiyambire cha ubwana wako.
Onse adzamwazika ndi mantha,
sipadzakhala ndi mmodzi yemwe wokupulumutsa.”
Copyright information for NyaCCL